Lero tiyeni tikavotele atsogoleri oti azathandiza dziko lathu. Afunseni ambuye mulungu kuti akutsogoleleni pamene mukukapanga chigamulo chimenechi chifukwa mukalakwitsa, muzamva kuwawa kwa m’bebe. Dziko ili likufunika mtsogoleri woti amakonda anthu ake.
#malawi #malawi2025 #elections
Ndiye, tiyeni tivotele mtsogoleri wina, osati anthu oti atiwonetsa kale kuti ndi atsankho, ozikonda, ankhwilu, aziphuphu, abodza ndipo obweretsa chisokonezo. Atsogoleri achoncho ndi oyipa, sangathe kutsogolera dziko bwino bwino, ndipo ambiri a choncho anatiwonetsa kale kuti ndi wolephela.
Onse amene adayesapo kale ma udindowa, ndipo sanapange zinthu bwino mmene analonjezela kalelo, bwino nawo, atipweteka!
Tiyeni aMalawi tiyese zina zanyuwani, tiyeni tipeleke voti kwa ena oti makhalidwe awo ndi zochita zawo zikuwonetsa kuti ndi anthu wokonda anthu amalawi wonse, olimbikila ndipo ndi wobweretsa anthu limodzi, osati opasula ndi a tsankho.
Chonde osawononga voti kuvotela atsogoleri a tsankho ndi a nkhwilu
#MALAWIDECIDES2025 #MALAWIELECTIONS2025
